I see my hand as the most stubborn part of my body, for sometimes it writes what my heart doesn't desire
Friday, October 02, 2009
Mayimbidwe apusitsa
Mayimbidwe apusitsa
Wolemba: ANANIYA ALICK PONJE
Mawu amene Yohane adawamva kuchokera mnyumba yomwe idayandikana ndi nyumba yake adali ozuna m’mapirikaniro mwake. Zidangokhala ngati woyimba nyimboyo adali mngelo wotsika kuchokera kumwamba. Mawu ake adali a nthetemya ngati a mwana wa mbalame ndipo akamayimba nyimbo yakeyo Yohane adalakalaka kuti woyimbayo azingoyimbabe.
Adaganiza zoti apite kunyumba komwe kunkachokera mawuwo ndi cholinga choti akathe kucheza komanso mwina kupalana ubwenzi ndi woyimbayo yemwe Yohane sadakayike kuti adali mtsikana wokongola ngati dzuwa. Chomwe Yohaneyo amadziwa chidali choti mnyumba yoyandikana ndi yakeyo mmene mmachokera mayimbidwe okomawo mudalowa mzimayi winawake masiku atatu apitawo. Sadaonepo mtsikana wina aliyense pamalopo komabe adadzitsimikizira yekha kuti mwina mtsikanayo adali atangofika kumene.
Poyamba Yohane adaganiza kuti woyimbayo adali mzimayi yemwe adamuthandiza kulowetsa katundu mnyumbamo koma adazindikira kuti sadali iyeyo atamva kuyimbako ngakhale pamene mziwayi adali panja pa nyumba akutsuka mbale. Sadafune kufunsa funso lirilonse mzimayiyo lokhuzana ndi munthu wodalitsidwa ndi mphatso yamayimbidweyo. Iye adaganiza kuti adapite kunyumbako mzimayiko akapita kuntchito ndi cholinga choti apeze mpata wokwanira kuti acheze ndi namwali woyimba mogometsayo.
Mmalingaliro ake adaona kamtsikana kokongola kolapitsa katakhala mnyumba mwake ndiponso kakumwetulira ngati duwa longomasula kumene. Mtima wake udadumphadumpha ndipo adangogwedeza mutu wake wopanda nyanga atadzidzi ndikuzindikira kuti zokoma zonsezo zidali malingaliro chabe. Adaganiza zoti akakumane ndi namwali woyimba ngati mbalame za mmunda wa Edeni mawa lake ndi cholinga choti adziwane bwinobwino ndiponso kuti mwinanso amuuze mawu a chikondi ngati kudali koyenera kutero.
Adayima pafupi ndi zenera la kuchipinda kwake ndikumamvetsera mayimbidwe okoma ochokera ku nyumba ija. Panopa zidangokhala ngati woyimbayo wawakonza mawu aja kokwana kasanu. Amamveka ngati kuti akuchokera muchoyimbira chongogulidwa kumene.
Mmawa mwake Yohane adalimba mtima. Atakhala pakhonde la nyumba yake kwakanthawi adaganiza zopita kunyumba komwe kumachokera mayimbidwe okoma kuja omwe panthawiyo adali ataleka. Adayenda mwakachetechete ngati mlenje woopa kuvumbulutsa nyama kuthengo.
Atatsala pang’ono kuti afike pakhomo lanyumbayo Yohane adaganiza zoti abwerere. Thupi lake lidali lodzadzidwa ndi chikayiko. “Ndikayamba bwanji popeza namwaliyo wasiya kuyimba. Bola akadakhala kuti akuyimbabe ndikadamulowa ndiyomuyamikira kuti amayimba bwino. Nanga pano ndikafika ndiyotani?” adaziyankhulira yekha Yohane.
Adabwereradi ndipo atangofika pakhomo la nyumba yake kuyimba koziziritsa mtima wa mwamuna wolusa ngati mkango wa njala kudayambanso ndipo panopa kumamveka pamwamba kwambiri ngati kulira kwa mwana wakhanda. Timawu ta woyimbayo tidali todzala ndi ulemerero.
Yohane adavutika kwambiri tsiku limenelo. Usiku udafika mochedwa kwambiri moti maola awiri adangokhala ngati mulungu wathunthu. Malingaliro a mmene mtsikana woyimbayo angakhale mkazi wachikondi chosasimbika adampangitsa Yohane kuyiwala kuti adali ndi bwenzi lake kumudzi lomwe adagwirizana nalo kale kuti adzamanga nalo banja. Iyeyo adaganiza kuti imeneyo siidali nthawi yomalimbana ndi atsikana a kumudzi omwe kwa iyeyo adali osasamba ndipo adalitchayira lamya bwenzi lakelo kuliuza kuti chibwenzi chawo chatha.
Adali atabwera kutawuniko zaka ziwiri zapitazo ndipo sadaganizepo zofuna kumusiya Nganile, mkazi yemwe ngakhale makolo kumudzi amadziwa kuti ndi amene atadzasamale mwana wawo, koma lero maganizowo adamubwerera. Adasiya nkhwali atamva kulira kwa kwa nkhanga.
Tsiku limenelo kudacha bwino ndipo kadzuwa kamawala mwa apo ndi apo. Nakonso kamphepo kayaziyazi kamaomba moyiwalitsa mavuto. Yohane adali limodzi ndi namwali wa mayimbidwe ozuna uja ndipo awiriwo adayamba kucheza.
“Dzina lako ndani?” adafunsa Yohane.
Ndipo mtsikanayo adayankha kuti dzina lake lidali Lusungu. Adaonjezeranso kuti adali ndi zaka makumi awiri. Yohane adangoti laponda lamphawi. Amangosiyana chaka chimodzi ndi iyeyo ndipo Yohane adaganiza kuti uyu ndiye adali mkazi woti amange naye banja.
“Lusungu ndimafuna ineyo ndi iweyo timange banja,” adayankhula mosapsyatira Yohane koma Lusungu asadayankhe Yohaneyo adadzidzimuka. Adali maloto chabe.
Mawa lake Yohane adalimba mtima ngati Davide pamaso pachimphona cha ku Filisiti ndikupita kunyumba komwe kumachokera mayimbidwe ozuna aja. Maloto amene adalota usiku wathawo adamulimbitsa mtima. Kuyimba kudali kumveka ndipo Yohane adagogoda pachitseko motsitsa. Kuyimba kuja kudasiya ndipo chitseko chidatseguka. Patsogolo pake padayima nkhalamba yomwe mmutu mwake mudali mutayereratu ndi imvi. Yohane adakhumudwa kotheratu. Nthawi yonseyo adangodikira madzi a mphutsi.
“Ndimati ndikuyamikireni kuti mumayimba bwino,” adayankhula Yohane mwamanyazi kuyiwuza nkhalamba ija.
“Zikomo kwambiri,” idayankha nkhalamba ija ndipo isadamalize kuyankhula Yohane adaliyatsa liwiro lobwerera kunyumba kwake. Adangofika ndi kudziponya pampando. Kuyimba konzuna kuja kudali kumvekabe. Adasiya bwenzi lake lakumudzi chifukwa chomva mayimbidwe okoma amunthu yemwe adali asadamuone. Adataya nkhwali chifukwa chongomva kulira kwa nkhanga.
Subscribe to:
Post Comments (Atom)
New data offers hope on HIV treatment
New data which a London-based pharma company, ViiV Healthcare, and a Geneva-based non-governmental organisation, Medicines Patent Pool (MPP)...
-
New data which a London-based pharma company, ViiV Healthcare, and a Geneva-based non-governmental organisation, Medicines Patent Pool (MPP)...
-
UNIMA introduces medical scheme (THIS ARTICLE WAS PUBLISHED IN THE NATION WITH SOME EDITING) By ANANIYA ALICK PONJE The University of Malaw...
-
Patriotism often means much more where one exercises it when he knows he has power to discount it. Its fruits stand the test of time where o...
No comments:
Post a Comment