Friday, October 02, 2009

Ndakatulo: Undilole

Undilole iwe m’Malawi
Amene uwonetsa khalidwe loyipa
Pochotsa kukongola kwachilengedwe
Komwe Namalenga analininkha
Dziko lokongola lino la Malawi
Undilole kuti ndikudzudzule mosapsyatira
Chifukwa chodula mitengo
Yokongoletsa Malawi wathu Undilole.

Undilole iwe m’Malawi
Woyipitsa fuko lako
Pogwirira tiana tongosiya kumene kuyamwa
Pokhalira malo amodzi ndi chipaso chako
Wasautsiranji dziko iwe m’Malawi
Wasautsiranji mtendere wa Malawi

Undilole kuti ndikumasule
Kuti ndikuuze choonadi undilole
Popeza wanyanzitsa dziko lako
Dziko la mtendere la Malawi
Undilolebe iwe m’Malawi
Wosanyadira uMalawi wako
Taona ulakalaka utakhala mzungu
Nunyoza zakwanu kuMalawi
Zodzala ndi kunzuna kwachilengedwe

Undilole nditsutsane nawe
Kuti mayiko ndi onse
Koma kwanu ndi kuMalawi
Ku Malawi dziko la mtendere.
Undilolenso iwe m’Malawi wopanda chikondi
Wofuna kukolola posalima
Iwe m’Malawi wa ulesi
Wofwamba olimbikira
Wopanda chikondi
Cholamulidwa ndi Leza wam’mwambamwamba
Iye wofuna iwe uleze mtima
Nanga bwanji uchotsa lamulo
Lokonda mzako monga udzikonda mwini
Koma undilole ndikudzudzule
Kuti Malawi wathu akhalebe Malawi wamtendere.

No comments:

New data offers hope on HIV treatment

New data which a London-based pharma company, ViiV Healthcare, and a Geneva-based non-governmental organisation, Medicines Patent Pool (MPP)...