Monday, June 15, 2009

NTHANO

Chilichonse chili ndi mphoto yake Nthano. Wolemba: Ananiya Alick Ponje Wogwirizira udindo wa mphunzitsi wamkulu pa sukulu ya Chandimana atamuyitanira Penjani m’kachipinda komatako, iye adadziwiratu kuti patelera. M’kachipindamo momwe nthawi zonse mumayalidwa carpet yofiira ngati magazi simunali moti mwana wa sukulu kulowamo chisawawa. Mapilikaniro a penjani atangolandira uthenga woti Penjaniyo akufunidwa ndi wogwirizira udindo wa m’phunzitsi wamkuluyo adamva kuwawasa m’kamwa mwake. Adayesa kusinkhasinkha kuti mwina ubongo wake womwe udali utamwazikana kale ungathe kukumbukira tsiku kapena nyengo imene adachita chinachake chomwe chidaputa m’kwiyo wa mphunzitsiyo, koma ngakhale kuti tiziduswa ta ubongo wake tidali titabwerera pamodzi, sadathe kukumbukirabe. Mkachipindamo munali wogwirizira udindo wa mphunzitsi wa mkulu uja komanso mphunzitsi wina yemwe adali ndi udindo woonesetsa kuti ana pasekondale ya Chandimana amakhala a makhalidwe abwino nthawi zonse. “Takuyitana muno ndi cholinga chimodzi ndipo tikukupempha kuti ukhale womasuka,” adayamba choncho wogwirizira udindo uja, akumezera malovu. Nkhope yake imanyezimira ndi ukali. “Tikufuna iwe ufotokoze mosachotsera kapena kuonjezera chimene ukudziwa pa nkhani yoti anyamata amafolomu ena mukumazunza ana a folomu wani.” Mtima wa penjani unagunda moopseza kuphwasula nthiti zake. “Ine ndisaname, sindikudziwapo kanthu.” “Penjani, usatichedwetse wamva. Tafotokoza mwachangu. Nthawi tilibe,” adatero akumuyang’ana mphunzitsi mzake uja yemwe amayenera kukhala patsogolo malinga ndi kuti nkhani yonseyo imakhuza chigawo chomwe iyeyo anali ndi udindo wotsogolera. “Ndikunena zoona aphunzitsi. Ine chibwerereni pasukulu pano, sindidayambe ndazunzapo mwana wa form 1 ngakhale m’modzi yemwe. Ndikudabwa kuti amene wakuuzaniyo amaganiza chiyani,” adadandaula Penjani. “Ife sitidanene kuti umazunza ana ndiwe koma timangofuna kuti unene chimene ukudziwapo iweyo. Pano ndiye wangodzipachika wekha. Ukuona, palibe chinsinsi padziko la pansi. Iweyo umaona ngati ukubisala. Ndiye ife titani poti waziyang’anitsa wekha ng’ombe ngolo? Tifunenso umboni wina?” adayankhula mtima uli zii. Penjani adayesa umu ndi umo kuti afotokoze bwinobwino koma sadapatsidwe mwawi wotere. Zoyankhula zake zimangolowera khutu lina la wogwirizira udindo wa mphunzitsi wamkuluyo n’kutulukira khutu lina. Mphunzitsi wina uja adayesesa kumuuza mphunzitsi mzakeyo kuti angompatsako mpata mwana wasukuluyo kuti afotokoze mbali yake koma mawu ake sadaphule kanthu. Adatemetsa nkhwangwa pamwala wogwirizira udindoyo. Adali wolimba mtima ngati wofula agalu. Ndipo pomaliza penipeni, wogwirizira udindoyo adamulembera Penjani kalata yomudziwitsa kuti wachotsedwa sukulu chifukwa chosowetsa mtendere ana a folomu yoyamba pasukulu ya Chandimana. Mkatalatamo, adasindika kunena kuti nkhani yonse idali itatumizidwa ku unduna wa zamaphunzira kuti undunawo upereke maganizo ake pankhaniyo “Koma mukadangondipatsa mpata woti ndifotokoze mbali yanga…” Penjani amadziwa kuti mwana akachotsedwa sukulu pa Chandimana, sizimatheka kuti abwererenso. Adakhetsa misozi ngati mwana wopsa ndi moto. “Choka. Tuluka muno. Chitsiru chimaphwasula tsogolo lake ndi manja ake. Ndikukutsimikizira kuti tsogolo lako lathera pano,” adanena monyogodola mphunzitsi wogwirizira udindo uja. “Koma aphunzitsi, zoona mungangondichotsa sukulu popanda chifukwa chenicheni. Bwanji mukadandiuza mwana yemwe ndinamuzunza.” “Nthawi imeneyo tilibe.” Pansi pamtima wake, woagwirizira udindo wa mphunzitsi wamkulu uja amadziwa kuti Penjani sadalakwe china chilichonse. Cholinga chomuchotsera sukulu chidali choti apeze mpata wolowetsera mwana wina polandira ziphuphu. Adali akuchita khalidwe limenelo kwa zaka zingapo ndipo pano lidali litamulowa m’magazi. Pasukulu ya Chandimana, boma lidalamula kuti mufolomu ina iliyonse musamapitirire ana makumi asanu ndi atatu. Ndipo mphunzitsi wogwirizira udindoyo amangochotsa ana pasukulupo pa milandu yosadziwika bwino. Penjani ataganiza zoti akawauze makolo ake, mutu wake udakula ngati wa kadzidzi. Adagwida ndi mantha ngati fisi wocheredwa mkhola la mbuzi. Iye amadziwa kuti amayenera kuchitapo kanthu. Kadali koyamba kuti aganize zobwezera chipongwe chachikulu m’moyo wake. Ataganiza njira iyi ndi iyo yobwezera chipongwecho adadzitsimikizira yekha kuti chisakhale chipongwe cha pathupi. Adangoganiza zopita ku ofesi ya wothandiza anthu olakwiridwa mnjira zosiyanasiyana ya ombudsman. Atafotokoza zonse, mkulu wa muofesiyo adakonza tsiku lodzamva mbali ya mphunzitsi wogwirizira udindo wa mphunzitsi wamkulu uja. Nkhani yonse itaunikidwa monzama, pamapeto pake mphunzitsi uja adapezeka wolakwa pochotsa sukulu ana opyola makumi awiri. Zidaululikanso kuti mphunzitsiyo adalowetsanso ana ena opyola makumi awiri polandira ziphuphu. Mlandu wa mphunzitsiyo udakazengedwa ku bwalo la milandu la Kanyenjere kumene woweruza adampeza mphunzitsiyo wolakwa pamulandu wolandira ziphuphu komanso mulandu wochotsa sukulu ana osalakwa. Milandu yonseyo idamuyitanira mphunzitsiyo zaka zisanu kundende komwe adakagwira ntchito yakalavula gaga. Ntchito ya uphunzitsinso idathera pompo ndipo ana ochotsedwa sukulu aja adabwezeretsedwa.

No comments:

New data offers hope on HIV treatment

New data which a London-based pharma company, ViiV Healthcare, and a Geneva-based non-governmental organisation, Medicines Patent Pool (MPP)...