Monday, June 15, 2009

NTHANO - AKOMA AKAGONERA

Penjani adadzambatuka pa kama pamene adagona ndi kuyamba kumwanza maso ake uku ndi uko ngati mfiti yopezereredwa ikutamba dzuwa likuswa mtengo. M’chipindamo mudali mowala bwinobwino chifukwa cha magetsi amphamvu amene adalimo, choncho padalibe malo oti mkazi wake angabisalemo. Ichi chidampangitsa Penjani kuti adzivomereze yekha kuti nthiti yakeyo siidali mchipindamo.

Zimene adaonanso m’zipinda zinazo zidali zoti zikadatha kuzunguza mitu ngakhale mikoko yogona. M’chipinda chogona alendo zinthu zambiri zimene Penjani adagula atangoyamba kumene ntchito zidali zitachotsedwamo. Zogonera komanso makina a kompyuta amene adali m’chipindamo dzulo dzuloli munalibe.

M’chipinda chinacho ndiye mudangokhala ngati bwalo losewerera mpira. Katundu wosiyanasiyana kuphatikizapo zikwama zitatu zimene Penjani adagula mudalibe.

Mutu wa Penjani udayimiratu atabwerera m’chipinda momwe amagona ndi mkazi wake. Poyamba pompaja sadathe kuona kuti chikwama chake chodzadza ndi zovala komanso ndalama zankhaninkhani chatengedwanso. Mwana wa mwamuna adalira ngati kuti kwagwa chauta.

Chimamuchitikira chidali chiyani? Line, nthiti yake yokondedwa yomwe idalonjeza paguwa pamaso pa anthu onse kuti idzakhala naye kufikira imfa ingachite zimenezo?

Mafunso opanda mayankho adasowetsa mtendere ubongo wa Penjani. Ataganiza za ndalama zankhaninkhani zomwe adaononga pokonzekera ukwati wawo, misonzi idayenderera m’maso mwake ngati mitsinje iwiri yoyandikana. Mtima wake udapitiriza kuvutika ndi maganizo a ndalama zimene adaononganso pogula katundu wodula yemwe adatengedwa ndi Line.

Adakumbukira mawu amene makolo ake adamuuza atapita kumudzi kukawonetsa mkazi wodzasunga moyo wake, ndipo adangolilira kuutsi. Adakumbukiranso malangizo ambirimbiri omwe anthu akufuna kwabwino adamuuza amene iyeyo adangowatenga ngati zokamba za akapasule.

"Mwana wanga Penjani, wachita bwino kubwera kuno kumudzi kudzationetsa mzako amene ukuganiza kuti ungathe kudzakhala naye moyo wako wonse, pamavuto ndi pamtendere," adayamba choncho mayi ake a Penjani.

"Panona ndikudziwa kuti ndiwe munthu wamkulu ndipo umaganiza mozama. Chomwechonso, ndikhulupirira wasankha bwino. Malemba oyera amanena kuti wopeza mkazi wapeza chinthu chabwino ndipo ndi wokonderedwa ndi Mulungu. Sindikufuna kutsutsana ndi malembawa koma ndingofuna kuti ndikudziwitse kuti kupeza mkazi ndi chinthu chabwino, koma sizitanthauza kuti aliyense wopeza mkazi amapeza mkazi wabwino."

Penjani adagwedeza mutu wake kuvomerezana ndi mayi ake.

"Mkazi wabwino angampeze ndani, malemba amateronso. Mkazi wabwino ndi amene amapatsidwa ndi Yehova."

"Zikomo kwambiri chifukwa cha malangizo anu amayi. Mwina ndingoyankhulapo ababa musanayankhule," adatero Penjani akuwayang'ana bambo ake. "Ine pofika pamaganizo obwera kumudzi kuno kudzaonetsa mkazi wanga ndinali nditaganiza mozama."

"Mwakhala nthawi yayitali bwanji muli pachibwenzi?" bambo ake a Penjani adamufunsa mwana wawo.

"Miyezi iwiri."

"Iwe ukuwona ngati miyezi iwiri ndi nthawi yoti mwamuna angakhale kuti wamudziwitsitsa mkazi? Ine ndi mayi ako tidakhala pachibwenzi kwa zaka zitatu komabe timaona ngati tapupuluma."

"Koma ino ndi nthawi ina. Mkazi amaonedwa ndi amuna ambiri."

"Chimenecho ndiye chifukwa chokwanira kuti anthu azitenga nthawi asanakwatirane. Mwana wanga, kuona maso ankhono n’kudekha. Kukhalitsa muli pachibwenzi ndi chinthu chimodzi chimene chingapangitse kuti awirinu mudziwane bwinobwino. Chimene ungadziwe n’chonena kuti ngati mkazi amaonedwa ndi amuna ambiri ali pachibwenzi, palibe choletsa kuonedwa ndi amuna ambiri ali pabanja."

"Chabwino mwachidule ndingonena kuti mkazi ndabwera nayeyu ndi wamakhalidwe abwino ndipo ndakhutitsidwa naye," adayankhula choncho Penjani.

"Mwana wanga, galu wamkota sakandira pachabe. Ife sitingangonena zonsezi, taziona zikuchitika. Akuluakulu ndi m’dambo mozimira moto," adayankhulanso mayi ake a Penjani.

Bambo ake nawonso sadasiyire pompo koma kupitiriza kuyankhula motere: "Kukula kumabweretsa nzeru zoti mnyamata ngati iwe sangakhale nazo. Angafupike bwanji, munthu wamkulu amatha kuona zobisika kuseri kwa phiri zoti mnyamata sangathe kuziwona."

Penjani adakhala ngati akumvetsera mwachidwi.

"Taona china chake mwa mkazi wako uja chimene chatidodometsa. Kayankhulidwe kake, mavalidwe ake, komanso kayendedwe kake ndi zinthu zoti zikukamba nkhani yopatsa chidwi kwambiri. Mosapsatira ndikuuze kuti mkazi amene uja sadzakusunga."

“Ngati nkhani yake ndi imeneyo, ndiye sitigwirizanapo pano.”

“Chisankho choti tigwirizane kapena tisagwirizane chili m’manja mwako. Ayankhula mawu amenewa ndi bambo ako ndipo akudziwa bwinobwino m’mene moyo wa m’banja umakhalira.”

Penjani adawayang’ana mayi ake mowaderera.

“Zovuta m’banja sizilephera, koma zisakhale chifukwa choti sudasankhe bwino.”

“Mwayankhula bwino. Zovuta sizilepheradi. Zovuta ndi zimene zimasemphanitsa amuna enieni kwa anyamata.” atayankhula mawu amenewa, Penjani adasanzika makolo ake ndi kupita m’chipinda momwe mudali mkazi wake.

Tsiku la chinkhoswe litafika, Penjani adayitanidwa pambali ndi akuluakulu ena omwe amaudziwa bwino moyo wa m’banja ndipo amafuna amupatse Penjaniyo malangizo okhuzana ndi moyo wa m’banja.

“Mkazi wabwino angampeze ndani?” adayamba choncho m’modzi wa alangiziwo. “Koma wopeza mkazi wapeza chinthu chabwino. Kunja kuno kuli akazi ambiri; okongola ngati dzuwa, oyenda ngati akuvina, oyenda osavala, ongofuna kubera amuna ndi ena otere.”

Anzake a mulangiziyo adamuvomereza mzawoyo pogwedeza mitu yawo.

“Mkazi wabwino angampeze ndani? Ndikhulupirira achimwene mwapeza mkazi wabwino. Koma simunganeneretu popeza mtima wa mzako ndi tsidya lina.”

“Mukuoneka kuti muli ndi mawo oposa zimene tikuganiza kuti mukutanthauza,” mzake m’modzi adayankhula.

“Mawu ndi omwewa, koma wanzeru ndi amene atanthauzira mawu kuposa kumvetsa kodziwikiratu. Wanzeru amatanthauzira china chilichonse choyankhulidwa ndi munthu wamkulu kuposa tanthauzo lapamwambamwamba,” adatero a Masikini, kenaka adapereka mpata kwa anzawo kuti ayankhuleponso.

“Wopeza mkazi wapezadi chinthu chabwino,” m’bwalo mudalowa mlangizi wina dzina lake Amonike. “Koma makamaka wopeza mkazi wabwino ndiye wodala kwambiri, poti akazi ndi onse…”

Penjani adadzuka pamene adakhala ndi kuyima chiriri. Sadayembekezere kuti omulangiza angayankhule zimenezo zimene m’kuganiza kwake sizimakhuzana ndi moyo wa m’banja. “Ndikhulupirira mwayankhula zimene mumafuna kuyankhula,” adatero, akunyatsitsa nkhope yake.

“Tamalizadi koma ukakhala ndi nzeru utanthauzira mwakuya. Sitinafune kuchulukitsa gaga mdiwa. Mawu onse obisika muzimene tayankhulazi uwalingalire mozama usanakatenge malumbiro paguwa.”

“Chabwino ndamva. Ndikhulupirira ndine womasuka.” Adatuluka m’chipindamo.

Penjani adalandire malangizo ankhaninkhani omuchenjeza kuti mkazi wake sakali ndi cholinga chofuna banja, koma kungomubera koma iye adatemetsa nkhwangwa pamwala kuti sangatayirane naye mkaziyo. Sadathe kulingalira malangizowo. Akanatha bwanji kutero atakutidwa ndi chikondi choyiwalitsa mwamuna kwawo chochokera kwa Line?

Akadatha bwanji mwana wa mwamuna timawu ta Line tokoma ngati uchi titamunong’oneza kambirimbiri kuti padziko lonse padalibe mwamuna winanso koma iye yekha?

Tsiku la ukwati, mbusa wokwatitsa ukwatiwo adafunsa ngati padali munthu amene adali ndi zifukwa zokwanira kuti awiriwo asamange woyera. Mzibambo wina wake wachikulire adadzuka pamene adakhala ndi kunena kuti adali nacho chifukwa cholepheretsa ukwatiwo. “Mkaziyo amagwira ntchito m’bala asanabwere kuno. Simkazi woti mwamuna n’kumamtenga ngati mkazi wako.”

Atamva mawuwo, Line adanamizira kukomoka. Cholinga chake chidali choti anthu amuone ngati kuti wakhuzidwa koopsa ndi zoyankhula za bamboyo yemwe amaoneka kuti amachokera kopapira bibida. Amafuna anthu akhulupirire kuti sadali wachimasomaso.

Mbusa adapitirizabe ndi ntchito yake Penjani atamuuza kuti mzibambo uja adali wokhuta gamazula ndipo samayenera kukhulupiriridwa.

“Malemba anena m’nyengo ino monga adatero kale: mkazi wabwino angampeze ndani? Wopeza mkazi wapeza chinthu chabwino. Koma si onse opeza akazi amapeza akazi abwino.”

Penjani, kuphatikizapo anthu ena ambiri omwe adali m’tchalichimo adali odabwa ndi zoyankhula za mbusayo. Chimene iwo amadziwa n’choti nthawi ya ukwati mbusa amanena kuti: “Banja ndi chinthu chokhazikitsidwa ndi Mulungu, choncho munthu sayenera kuphasula chomangidwa ndi mwini wake Yehova.”

Penjani adaganiza kuti zoyankhula zonse zimene adazimva kuchokera kwa anthu ambirimbiri zokhuzana ndi banja zimayenera kukhala ndi matanthauzo oposa m’mene amaganizira. Koma chifukwa chomukondetsetsa Line, adamangitsabe ukwati uja.

Atakhala milungu iwiri yokha ali limodzi mbanja ndi m’mene amadzidzimuka usiku umenewo kuona kuti Line wathawa ndi katundu wochuluka kwamnanu. Zidatheka bwanji Penjaniyo kugona tulo mpaka kukanika kudzuka nthawi imene katundu wankhaninkhaniyo amatutidwa? Nanga katunduyo adanyamulidwa pa chiyani? Awa adali ena mwa mafunso omwe adamuzinga Penjani.

No comments:

New data offers hope on HIV treatment

New data which a London-based pharma company, ViiV Healthcare, and a Geneva-based non-governmental organisation, Medicines Patent Pool (MPP)...